Khonsolo ya Mzinda wa Zomba Igwilana Manja ndi Dodma Pofalitsa Malamulo Atsopano
14,Aug 2025
Posted By : Aubrey Mthyola
0 Comments
Khonsolo ya mzinda wa Zomba yati igwira ntchito pamodzi ndi nthambi yoona zangozi zogwa mwadzidzidzi ya Dodma pofalitsa malamulo atsopano okudza ngozi zogwa mwadzidzidzi (Disaster Risk Management Act, 2023) kwa anthu okhala mu mzinda wa Zomba.
Mkulu oona zangozi zogwa mwadzidzidzi ku khonsolo yamzinda wa Zomba, Gomezgani Nyasulu wati malamulowa akupereka mphamvu ku khonsolo pakagwilidwe ntchito zokhudza ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Nyasulu wati pakadali pano khonsolo yaika kale ndondomeko zomwe zithandize kufalitsa malamulowa monga kudzera pawailesi, mikumano ndi anthu akudera ndi chimkuza mawu.
Nyasulu: Takonzeka kutumikira ndi nyonga
Polankhula pamtsiliziro wa mkumano omwe Dodma inachita ndi adindo oona zangozi zogwa mwadzidzidzi, a Clement Chafulumira a ku Dodma anati malamulowa akukhudza zigawo zambiri.
Iwo anati mwazina malamulowa akukamba za malo achiopsezo ndi ndondomeko zomwe zaikidwa ndi boma kutianthu okhala malo otere asamukile malo otetezeka.
Chafulumira: Anthu okhala malo achiopsezo akuyenera kusamuka